09/12/2026
Akulu Akulu Ndende Za Ku Malawi Kuno Kuli Anthu Okuti Adamangidwa Court Silinawapeze Olakwa Komaso Zoti Mlandu Wawo Udzalowa Liti Sakudziwa. Koma Akutha Zaka.
Anthu Ena Akagwidwa Sachedwa Koma Kutumizidwa Ku Maula Ndipo Mboni Ya Boma Imachita Kupempha Kumpando Kuti Apatsidwe Chilango Chachikulu.
Pamene Anthu Ena Milandu Yawo Ikumalowa Mu Court Kutuluka Kusinthidwa Date Kudzalowaso Nkusinthidwaso Date
Ena Mwayi Woti Nkhani Yawo Ikalowe Mu Court To Prove their Innocent Alibe .
Ena Milando Yomweyo Anamangidwa Akuseva Chi Sentence Ena Ndi Awa Tuwawona Mma Social Media wa.
Chonde Tiyeni Tikondane Tidziyika Chilungamo Patsogolo. Ku maula Amadya Kamodzi Nsima Pa Tsiku Ndipo Nyemba Amakhuthula Mpoto Mmene Adapakilira Mlimi ku Munda Kulibe zosankha Miyala.
Nde Kuti Udzikhala Kundende Usakudziwa Sentence Nzovetsa Chisoni. Adindo Tenganipo Gawo. Chilango Kumapeleka Chofanana Kwa Aliyese.
Osati Poti Ndi Awa Apatsidwe Belo Poti Ndi Awa Tisawamange abakachita Kaye Zina Ndekuti Chilungamo Sichiyenda Bwino.